29/08/2026
Tikambeko za utambwali wa amisili/crooked craftsmen.
Anthu ambiri a ntchito za manja monga a telara, azomangamanga, ma carpenter amatchuka ndi kusakhulipirika pa ntchito. Ntchito izizi nthawi zambiri zimafunika kuti munthu apeleke deposit yomwe imakhala ndalama yogulira materials kuti zotsalazo azapeleke ntchito ikatha ndipo akhutitsidwa.
Koma chomwe chimachitika ndi choti ambiri amapezeka kuti adya ndalama za customer osagula materials. Zimenezi zimapangitsa kuti ntchito ija ichedwe kapenanso isachitike. Izi zimaononga mbiri ya company.
Ambiri akabwela amati ndikufuna katundu oti ali ready kale zopeleka ma order ine ayi chifukwa cha zomwe anamvapo kapena kukumana nazo. Vuto ndi loti, sitingakhale ndi ma bed, ma dining set, ma TV stand a mitundu yonse nthawi zonse. Zinthuzi zimakhala mma design, sizes and colors zosiyanasiyana.
Ife timanena kuti customer ali omasuka kutiyendela tsiku lirilonse kuzaona mmene ntchito yake ikuyendela.
MALANGIZO KWA OGULA
Musanapeleke deposit pa order ya ndalama zambiri onesetsani kuti mwachita zina mwa izi:
1. Mwadziwa malo omwe anthuwo amapezeka komanso kugwilira ntchito yawo.
2. Yang’anani pa Facebook kuti muone kuti company yi ikuchokela kuti?. Panopa wa business wa serious akuyenela kukhala ndi page kapena website
3. Apanga business nthawi yaitali bwanji?
4. Onaniko ka sample ka ntchito yawo yoti inatha kale kuti mudziwe zomwe mukuyembekezela. Musaiwale, ena amapanga post pa Facebook katundu oti sanapange ndi iwowo.
Ka background check akaka katha kukupulumutsa ndalama zanu komanso kukupewetsani ma BP.
Tsiku lina tizakamba za ma customer opanda patience. Ma customer omwe amati ukawauza 10 days, usayelekeze kuphonya ndi 2 days mpaka ndalama zawo ubweza🙆🏻
Ngati mwapeza kuti ma tips awawa ndi othandiza, tidziwitseni popanga Like. Osaiwala kupanga follow TrippleS HomeStore pamene tipitilize kuunikilana zambiri zokhudza furniture.